jesus image

Tsono Mwalandira Yesu, Zofunika ndi zotani?...

Kodi Mwalandira Yesu
Kodi mudziwa bwanji kuti yesu alowa zoona? Mudziwa popeza ambuye Yesu analonjeza kuti adzalowa pamene mutsegula pa khomo ndikumuuza kuti alowe.  Ngati  mwapemphera ndi mtima woona, khulupirirani kuti Yesu alowa monga analonjeza.

Mau a Mulungu Aalonjeza Moyo Wosatha
"Ndipo uwu ndi ubwino, kuti Mulungu anatipatsa ife moyo wosatha, ndipo moyo umene uli mwa Mwana wace.  Iye wakukhala ndi Mwana ali nao moyo.  Izi nakulemberani kuti mudziwe kuti muli ndi moyo wosatha" (1 Yohane 5:11-13).

Yamikani Mulungu tsiku ndi tsiku cifukwa mwalandira Yesu Kristu ndiponso kuti iye anakupatsani moyo wosatha.  Yesu analonjeza kuti sadzakusiyani.   
Kodizina zofunika ndi zotani?

Otsaiwala ai...

Khulupirani Mulungu, Zina Zibwela M'mbyo
Mkristu ndi Munthu yemwe akhulupirira zomwe Mulungu alonjeza mu Mau ace.  Cithunzi-thunzi ici ca sitima (Train) cifotokozera m'mene coona ca Mau a mulungu, ndi cikhulupiriro cathu, ndi zina za bwino zobwera pambuyo, zigwirizana kuti tikhale ndi moyo weni-weni wabwino.

truck.gif (6955 bytes)

  1. Mphavu ili ndi Mulungu ndi Mau ace.
  2. Mwa Cikhulupiriro tilumikizidwa ku mphavu, imeneyo.
  3. Zina zotsimikizira kuti tapulumutsidwa, zibwera pambuyo.

Pamene Mwalandira Yesu Kristu...

Pamene mulandira Yesu Kristu mwa cikhulupiriro, izi zicitika mu m'moyo wanu:

  1. Yesu Kristu walowadi mu moyo wanu, ndiponso wakupatsani moyo wosatha (1Yohane 5:11-13).
  2. Macimo anu akhululikidwa (Macitidwe 10:43).
  3. Mzimu woyela amene wakhala mwa inu tsopano, akubadwitsani mwatsopano ndi kukutsinthani kukhala mwana wa Mulungu (Akolose 1:14: Yohane 1:12.).
  4. Mwabadwa mwatsopano kukhala ndi moyo weni-weni wabwino umene Mulungu wakupatsani (Yohane10:10 ndi Akorinto5:14-17).

Kodi pali dalitso lina loposa ili lomwe mukhoza kuzindikira kuti muli ndi moyo wosatha cifukwa Yesu Kristu anakuferani ndi kukupulumutsani?
  Kodi simufuna kuyamika Mulungu tsopano cifukwa ca cinthu cacikulu comwe akucitirani lero?  Kupemhera kusonyedza cikhulupiriro canu mwa Mulungu. 

Tsopano ticita ciani?


Tsopano Muyenera Kukula

Mudzakulabe mu umoyo wanu wa Cikristu ngati mucita zinthu izi:

    Pempherani Pempherani tsiku ndi tsiku (Yohane 15:7)
    Werengani Werengani Mau a Mulungu tsiku ndi tsiku (Macitidwe 17:11)
    Mverani Mverani Mulungu nthawi zonse (Yohane 14:31).
    Citirani Umboni Citirani umboni wa Ambuye Yesu ndi umoyo wanu wabwino ndi Mau ace. (Yohane 15:8; Mateyu 4:19)
    Khulupirirani Khulupirani Mulungu ndipo tulani nkhawa zanu zonse. (1 Petro 5:7) 
    Dziperekeni Dziperekeni tsiku ndi tsiku kwa Yesu Kristu kuti akhale mfumu wa zonse za moyo wanu ndipo mulole Mzimu Woyera ukutsogolereni ndi kukupatsani mphamvu. (Agalatiya 5:16, 17; Macitidwe 1:8)

Ncofunika Kulowa M'mpingo

Nkuni itakhala pa yokho, moto suyaka bwino.  Pafunika kuti ikhale ndi zinzace kuti moto uyake bwino. Motero inunso simungathe kukhala ndi moyo weni-weni wabwino panokha osayanjana ndi Akristu anzanu.

Muyenera kulowa mu mpingo kuti muyanjane ndi Akristu anzanu omwe analandira Mau a Mulungu.

Zina zomuthandizani kukula mu Cikristi.

Ngati mufuna kumva zina za moyo wa Cikristu ndi m'mene mungathe kuphunzira zina, tumani fomu, kapena lembani kalata ku  Campus Crusade for Christ-Zambia P.O. Box 36176 Lusaka, Zambia, ndiponso mungathe kutuma formu iyi.

ZOFUNIKA ZINA