jesus image

Kodi Yesu Ndi Yani?

Kodi Yesu wa ku Nazareti ndani kwani inu?  Yankho yanu ku funso iyi itha kusintha moyo wano onse kwa nthawi yosatha.

dove

Kwa inu kodi Yesu N'dani

  • Munthu opambana kwa nthawi zonse?

  • Mtsogoleri Opambana?

  • Mphunzitsi Opotsa?

  • Omwe acita zabwino kwa anthu onse?

  • Munthu anakhala moyo oyela kopotsa anthu onse?

 

Mungathe kupika ku dziko lililonse kapena kulankhula ndi anthu a mipingo yosina-siyana ngakhale ndi odzipeleka ku mupingo wao.  Komabe adzavomela kuti kulibe munthu wina opotsa Yesu Kristu waku Nazareti.  Moyo wace unali odabwistsa kwabasi.

KUBWELA KWAKE KUNALONJEZEDWA

Zikwi-zikwi, pomwe Yesu sanabadwe, Malembo Oyera atiudza za aneneli a Israyeli  akulonjeza kubwela kwa Yesu.  Cipangano cakale mu Buku Lopatulika, cinalembedwa ndi aneneri ambiri kwa dzaka zikwi khumi ndi zisanu kulonjeza kubwela kwace.  Zonse zomwe zinalembedwa dzinafikilisidwa.

Moyo wace, zodzidzitswa zace, mau ace, infa yace, ku-ukitsidwa kwa akufa kwace ndi kupita kumwamba kwace, zonse zisonyeza kuti Yesu anali mwana wa Mulungu.  Yesu anati "Ine ndi Atate tili m'modzi" (Yohane10:30), "Iye amene waona ine anona Atate" (Yohane 14:9). Yesu anati "Inen dine njira coonadi ndi moyo, kulibe obwela kwa Atate kopanda ine"  (Yohane 14:6).

MOYO NDI UTHENGA WACE

Onani moyo, uthenga ndi macitidwe a Yesu Kristu.  Anthu ambirir-mbiri akhala akusintha cifukwa ca moyo wa Yesu Kristu.  Kuli konse komwe uthenga ndi maphunzintso ace apita anthu amitundu yonse asintha.5000

YESU ANAUKA KWA AKUFA

Yesu Kristu anapacikidwa pa mtanda, naikidwa m'manda, ndipo tsuku yacitatu anauka kwa akufa.  Cikristu ndicodabwitsa cifukwa ca ku ukitsidwa kwa Yesu kristu.

Zaka zambiri zapitapo, ndipo anthu ophunzira ambiri azindikira ndi kucitira umboni kuti Yesu Kristu alimoyo."

John Singleton Copley, mtsogoleri wa opuhunzira ku mangalande anati, "Ndizindkila  kuti Yesu anauka kwa akufa ndipo zimenedzi sidzitsusidwa ayi."

NICIFUKWA NINJI TIKHULUPIRIRA?

Kuukisidwa kwa akufa kwa Yesus Kristu ndi kwakukulu kwa a Kristu aonse.  Ndipo ife tikhulupirira cifukwa ca izi: 

boatKUNALONJEZEDWA: Coyamba, Yesu Kristu mwini ananena za infa yace ndi ku-uka kwa akufa kwace pamene nthawi sinafike (Luka18:31-33)

MANDA ACE ANALIBE KANTHU:  
Caciwiri, m'manda momwe munaikidwa mtembo wace munalibe pa tsiku yacitatu.  Ici cisonyeza kuti Yesu anadzuka.  Baibulo limatiuza ife kuti asilikali anaikidwa kuonela manda ndipo cimwala cacikula cinaikidwa pakhomo pamandayo.  Mtembo wa yesu sinabedweayi, koma iye anauka kwa akufa.

ANAONEKELA KWA IWO:Cacitatu, Yesu Kristu anaonekela kwa omphunzira ace ndi kwa anthu ambiri-mbiri (500) pa nthawi imodzi, pamene iye anadzuka.  Yesu anaonetselatu kuti iye ndwmoyo ndipo iye anadya naocakudya.

KUBADWA KWA MUPINGO(CHALICI): Cacinai, kuuka kwa Yesu kristu kwa akufa ndiko kubadwa kwa mpingo (Chalici). Chalici ya Akristu ndi mpingo ukulu opambana pa dziko lonse lapansi .

MOYO WATSOPANO:  
Dziko lonse lapansi, anthu osiyana-siyana akhla akupeza mtendere pamena aika cikhulupiriro cao mwa Yesu Kristu.  Kulibe munthu atha kusintha moyo wa anthu monga Yesu kristu.  Zonsezi zicitira umboni ku coondi coti Yesu Kristu ali moyo lelo ndipo iye anauka kwa akufa.

jesusandgirlMFUMU YA MOYO:
Cifukwa cakuukitsidwa kwa Yesu Kristu kwa akufa, onse ophunzira ace akhulupirira muli Ambuye ndi Mfumu lamoyo.  Kalelo, Yesu alimoyo ndipo apatsa moyo weni-weni ndi ocuruka kwa yense okhulupirira mwa iye.  Ambiri avomela ndi kucitira umboni kuuka kwa Yesu Kristu ngakhale manfumu ndi atsogoleri ocukha pa dziko lapansi.


Kodi mungakonde kumudziwa Yesu Kristu, kuti iye akhale bwenzi lanu ndi kukupatsani moyo weni-weni ocuruka?  Yesu afunitsitsa kumupatsani Moyo ocuruka.

Ngati mufuna kuti Yesu akhale mpulumutsi ndi mtsogoleri wanu, dinizani apa...

ZOFUNIKA ZINA